Si nyengo yakumweta tirigu lero kodi? Ndidzaitana kwa Yehova, kuti atomize bingu ndi mvula; ndipo mudzazindikira ndi kuona kuti coipa canu munacicita pamaso pa Yehova ndi kudzipemphera mfumu, ncacikuru.