1. Ndipo ana a Rubeni mwana woyamba wa Israyeli, (pakuti ndiye mwana woyamba; koma popeza anaipsa kama wa atate wace ukulu wace unapatsidwa kwa ana a Yosefe mwana wa Israyeli, koma m'buku la cibadwidwe asayesedwe monga mwa ukulu wace.
2. Pakuti Yuda anakula mphamvu mwa abale ace, ndi mtsogoleri anafuma kwa iyeyu, koma ukulu ngwa Yosefe);
3. ana a Rubeni mwana woyamba wa Israyeli: Hanoki, ndi Palu, Hezroni, ndi Karmi.
4. Ana a Yoeli: Semaya mwana wace, Gogi mwana wace, Simei mwana wace,
5. Mika mwana wace, Reaya mwana wace, Baala mwana wace,