36. Ana a Elifazi: Teani, ndi Omara, Zefi, ndi Gatamu, Kenazi, ndi Timna, ndi Amaleki.
37. Ana a Reueli: Nahati, Zera, Sama, ndi Miza.
38. Ndi ana a Seiri: Lotani, ndi Sobala, ndi Zibeoni, ndi Ana, ndi Disoni, ndi Ezeri, ndi Disani.
39. Ndi ana a Lotani: Hori, ndi Homamu; ndipo Timna ndiye mlongo wace wa Lotani.
40. Ana a Sobala: Abiani, ndi Manahati, ndi Ebala, Sefi, ndi Oramu. Ndi ana a Zibeoni: Aiya ndi Ana.
41. Mwana wa Ana: Disoni. Ndi ana a Disoni: Hamirani, ndi Esibani, ndi Itrani, ndi Kerani.
42. Ana a Ezeri: Bilani, ndi Zavani, ndi Yakani. Ana a Disani: Uzi, ndi Arani.
43. Mafumu tsono akucita ufumu m'dziko la Edomu, pakalibe mfumu wakucita ufumu pa ana a Israyeli, ndiwo Bela mwana wa Beori; ndi dzina la mudzi wace ndilo Dinaba.
44. Ndipo anafa Bela; ndi Yobabi mwana wa Zera wa ku Bozra anakhala mfumu m'malo mwace.