Ndipo anacinga makoma a nyumba m'katimo ndi matabwa amkungudza, kuyambira pansi kufikira posanja, nacinga m'katimo ndi matabwa, nayala pansi m'nyumbamo matabwa amlombwa.