Ndipo Solomo anapatsa Hiramu miyeso ya tirigu zikwi makumi awiri ndiyo zakudya za banja lace, ndi miyeso makumi awiri ya mafuta oyera; motero Solomo anapatsa Hiramu caka ndi caka.