Ndipo kunali, atamva Yezebeli kuti anamponya Naboti miyala nafa, Yezebeli anati kwa Ahabu, Taukani, landirani munda wamphesa wa Naboti Myezreeli uja anakana kukugulitsani ndi ndarama, popeza, Naboti sali ndi moyo, koma wafa.