Ndipo taonani, mneneri anadza kwa Ahabu mfumu ya Israyeli, nati, Atero Yehova, Kodi waona unyinji uwu waukuru wonse? Taonani, ndidzaupereka m'dzanja mwako lero, kuti udziwe kuti ndine Yehova.