Tsono Farao anati kwa iye, Koma cikusowa iwe nciani kwa ine, kuti ufuna kumuka ku dziko la kwanu? Nayankha iye, Palibe kanthu, koma mundilole ndimuke ndithu.