Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 9:28-41 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Ndipo anamlalatira iye, nati, Ndiwe wophunzira wa Iyeyu, ife ndife akuphunzira a Mose.

29. Tidziwa ife kuti Mulungu analankhula ndi Mose; koma sitidziwa kumene acokera ameneyo,

30. Munthuyu anayankha nati kwa iwo, Pakuti cozizwa ciri m'menemo, kuti inu simudziwa kumene acokera, ndipo ananditsegulira maso anga.

31. Tidziwa kuti Mulungu samvera ocimwa. Koma ngati munthu ali yense akhala wopembedza Mulungu nacita cifuniro cace, amvera ameneyo.

32. Kuyambira paciyambi sikunamveka kuti wina anatsegulira maso munthu wosaona cibadwire.

33. Ngatiuyu sanacokera kwa Mulungu, sakadakhoza kucita kanthu.

34. Anayankha natikwa iye, Wabadwa iwe konse m'zoipa, ndipo iwe utiphunzitse ife kodi? Ndipo anamtaya kunja.

35. Yesu anamva kuti adamtaya kunja; ndipo pakumpeza iye, anati, Kodi ukhulupirira Mwana wa Mulungu?

36. Iyeyu anayankha nati, Ndipo ndani iye, Ambuye, kuti ndimkhulupirire iye?

37. Yesu anati kwa iye, Wamuona iye, ndiponso wakulankhula ndi iwe ndi Iyeyo.

38. Koma iye anati, Ndikhulupirira, Ambuye; ndipo anamgwadira iye.

39. Ndipo Yesu anati, Kudzaweruza ndadza Ine ku dziko lino lapansi, kuti iwo osapenya apenye; ndi kuti iwo akupenya akhale osaona,

40. Ndipo Afarisi ena akukhala ndi iye anamva izi, nati kwa iye, Kodi ifenso ndife osaona?

41. Yesu anati kwa iwo, Mukadakhala osaona simukadakhala nalo cimo; koma tsopano munena, kuti, Tipenya: cimo lanu likhala.

Werengani mutu wathunthu Yohane 9