Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 9:23-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Cifukwa ca ici atate wace ndi amace anati, Ali wamsinkhu; mumfunse iye.

24. Pamenepo anamuitana kaciwiri munthuyo amene anali wosaona, nati kwa iye, Lemekeza Mulungu; tidziwa kuti munthuyo ali wocimwa.

25. Pamenepo iyeyu anayankha, Ngati ali wocimwa, sindidziwa; cinthu cimodzi ndicidziwa, pokhala ndinali wosaona, tsopano ndipenya.

26. Cifukwa cace anati kwa iye, Anakucitira iweciani? anakutsegulira iwe maso bwanji?

27. Iye anayankha iwo, Ndinakuuzani kale, ndipo simunamva; mufuna kumvanso bwanji? kodi inunso mufuna kukhala: akuphunzira ace?

28. Ndipo anamlalatira iye, nati, Ndiwe wophunzira wa Iyeyu, ife ndife akuphunzira a Mose.

29. Tidziwa ife kuti Mulungu analankhula ndi Mose; koma sitidziwa kumene acokera ameneyo,

30. Munthuyu anayankha nati kwa iwo, Pakuti cozizwa ciri m'menemo, kuti inu simudziwa kumene acokera, ndipo ananditsegulira maso anga.

Werengani mutu wathunthu Yohane 9