Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 9:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo popita, anaona munthu ali wosaona cibadwire.

2. Ndipo akuphunzira ace anamfunsa iye, nanena, Rabi, anacimwa ndani, ameneyo, kapena atate wace ndi amace, kuti anabadwa wosaona?

3. Yesu anayankha, Sanacimwa ameneyo, kapena atate wace ndi amace; koma kuti nchito za Mulungu zikaonetsedwe mwa iye.

4. Tiyenera kugwira nchito za iye wondituma Ine, pokhala pali msana; ukudza usiku pamene palibe munthu angakhoze kugwira nchito,

5. Pakukhala Ine m'dziko lapansi, ndiri kuunika kwa dziko lapansi.

6. Pamene ananena izi, analabvula pansi, nakanda thope ndi malobvuwo, napaka thopelo m'maso,

7. nati kwa iye, Muka, kasambe m'thamanda la Siloamu (ndilolosandulika, Wotumidwa). Pamenepo anacoka, nasamba, nabwera alikuona.

8. Cifukwa cace anzace ndi iwo adamuona kale, kuti anali wopemphapempha, ananena, Kodi si uyu uja wokhala ndi kupemphapempha?

Werengani mutu wathunthu Yohane 9