Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 8:47-59 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

47. 6 Iye wocokera kwa Mulungu amva zonena za Mulungu; inu simumva cifukwa cakuti simuli a kwa Mulungu,

48. Ayuda anayankha nati kwa iye, Kodi sitinenetsa kun Inu ndinu Msamariya, ndipo 7 muli ndi ciwanda?

49. Yesu anayankha, Ndiribe ciwanda Ine; koma ndilemekeza Atate wanga, ndipo inu mundipeputsa.

50. Koma 8 Ine sinditsata ulemerero wanga; alipo woutsata ndi wakuweruza.

51. Indetu, indetu, ndinena ndi inu, 9 Munthu akasunga mau anga, sadzaona imfa nthawi yonse.

52. Ayuda anati kwa Iye, Tsopano tazindikira kuti muli ndi ciwanda. 10 Abrahamu anamwalira, ndi aneneri; ndipo Inu munena, Munthu akasunga mau anga, sadzalawa imfa ku nthawi yonse.

53. Kodi Inu ndinu wamkulu ndi atate wathu Abrahamu, amene anamwalira? ndipo aneneri anamwalira: mudziyesera nokha muli yani?

54. Yesu anayankha, Ngati Ine ndidzilemekeza ndekha, ulemerero wanga uli cabe; 11 Atate wanga ndiye wondilemekeza Ine; amene munena za iye, kuti ndiye Mulungu wanu;

55. ndipo 12 inu simunamdziwa iye; koma Ine ndimdziwa iye; ndipo ngati ndinena kuti sindimdziwa iye, ndidzakhala wonama cimodzimodzi inu; koma ndimdziwa iye, ndipo ndisunga mau ace.

56. 13 Atate wanu Abrahamu anakondwera kuona tsiku langa; ndipo anaona, nasangalala.

57. Ayuda pamenepo anati kwa iye, Simunafikire zaka makumi asanu, ndipo munaona Abrahamu kodi?

58. Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, asanayambe kukhala Abrahamu ndipo 14 Ine ndiripo.

59. Pamenepo 15 anatola miyala kuti amponye iye; koma Yesu anabisala, naturuka m'Kacisi.

Werengani mutu wathunthu Yohane 8