Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 8:32-52 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. ndipo mudzazindikira coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani.

33. Anamyankha iye, Tiri mbeu ya Abrahamu, ndipo sitinakhala akapolo a munthu nthawi iri yonse; munena bwanji; Mudzayesedwa aufulu?

34. Yesu anayankha iwo, nati, Indetu, indetu, ndinena kwa inu kuti yense wakucita cimo ali kapolo wa cimolo.

35. Koma kapolo sakhala m'nyumba nthawi yonse; mwana ndiye akhala nthawi yonse.

36. Cifukwa cace ngati Mwana adzakuyesani inu aufulu, mudzakhala mfulu ndithu.

37. Ndidziwa kuti muli mbeu ya Abrahamuj koma mufuna kundipha Ine, cifukwa mau anga alibe malo mwa inu.

38. 1 Zimene ndinaona Ine kwa Atate, ndilankhula; ndipo inunso mucita cimene mudamva kwa atate wanu.

39. Anayankha nati kwa iye, Atate wathu ndiye Abrahamu. Yesu ananena nao, 2 Ngati muli ana a Abrahamu, mukadacita nchito za Abrahamu.

40. Koma tsopano mufuna kundipha Ine, ndine munthu amene ndinalankhula ndi inu coonadi, 3 cimene ndinamva kwa Mulungu; ici Abrahamu sanacita.

41. Inu mucita nchito za atate wanu. Anati kwa iye, Sitinabadwa ife m'cigololo; tiri naye Atate mmodzi ndiye Mulungu.

42. Yesu anati kwa iwo, 4 Mulungu akadakhala Atate wanu, mukadakonda Ine; pakuti Ine ndinaturuka, ndi kucokera kwa Mulungu; pakuti sindinadza kwa Ine ndekha, koma Iyeyu anandituma Ine.

43. Simuzindikira malankhulidwe anga cifukwa ninji? Cifukwa simungathe kumva mau anga,

44. 5 Inu muli ocokera mwa atate wanu mdierekezi, ndipo zolakalaka zace za atate wanu mufuna kucita. Iyeyu anali wambanda kuyambira paciyambi, ndipo sanaima m'coonadi, pakuti mwa iye mulibe coonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wace; pakuti ali wabodza, ndi atate wace wa bodza.

45. Koma Ine, cifukwa ndinena coonadi, simukhulupirira Ine.

46. Ndani mwa inu anditsutsa Ine za cimo? Ngati ndinena coonadi, simundikhulupirira Ine cifukwa ninji?

47. 6 Iye wocokera kwa Mulungu amva zonena za Mulungu; inu simumva cifukwa cakuti simuli a kwa Mulungu,

48. Ayuda anayankha nati kwa iye, Kodi sitinenetsa kun Inu ndinu Msamariya, ndipo 7 muli ndi ciwanda?

49. Yesu anayankha, Ndiribe ciwanda Ine; koma ndilemekeza Atate wanga, ndipo inu mundipeputsa.

50. Koma 8 Ine sinditsata ulemerero wanga; alipo woutsata ndi wakuweruza.

51. Indetu, indetu, ndinena ndi inu, 9 Munthu akasunga mau anga, sadzaona imfa nthawi yonse.

52. Ayuda anati kwa Iye, Tsopano tazindikira kuti muli ndi ciwanda. 10 Abrahamu anamwalira, ndi aneneri; ndipo Inu munena, Munthu akasunga mau anga, sadzalawa imfa ku nthawi yonse.

Werengani mutu wathunthu Yohane 8