Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 8:31-43 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Cifukwa cace Yesu ananena kwa Ayuda aja adakhulupirira iye, Ngati mukhala inu m'mau anga, muli akuphunzira anga ndithu;

32. ndipo mudzazindikira coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani.

33. Anamyankha iye, Tiri mbeu ya Abrahamu, ndipo sitinakhala akapolo a munthu nthawi iri yonse; munena bwanji; Mudzayesedwa aufulu?

34. Yesu anayankha iwo, nati, Indetu, indetu, ndinena kwa inu kuti yense wakucita cimo ali kapolo wa cimolo.

35. Koma kapolo sakhala m'nyumba nthawi yonse; mwana ndiye akhala nthawi yonse.

36. Cifukwa cace ngati Mwana adzakuyesani inu aufulu, mudzakhala mfulu ndithu.

37. Ndidziwa kuti muli mbeu ya Abrahamuj koma mufuna kundipha Ine, cifukwa mau anga alibe malo mwa inu.

38. 1 Zimene ndinaona Ine kwa Atate, ndilankhula; ndipo inunso mucita cimene mudamva kwa atate wanu.

39. Anayankha nati kwa iye, Atate wathu ndiye Abrahamu. Yesu ananena nao, 2 Ngati muli ana a Abrahamu, mukadacita nchito za Abrahamu.

40. Koma tsopano mufuna kundipha Ine, ndine munthu amene ndinalankhula ndi inu coonadi, 3 cimene ndinamva kwa Mulungu; ici Abrahamu sanacita.

41. Inu mucita nchito za atate wanu. Anati kwa iye, Sitinabadwa ife m'cigololo; tiri naye Atate mmodzi ndiye Mulungu.

42. Yesu anati kwa iwo, 4 Mulungu akadakhala Atate wanu, mukadakonda Ine; pakuti Ine ndinaturuka, ndi kucokera kwa Mulungu; pakuti sindinadza kwa Ine ndekha, koma Iyeyu anandituma Ine.

43. Simuzindikira malankhulidwe anga cifukwa ninji? Cifukwa simungathe kumva mau anga,

Werengani mutu wathunthu Yohane 8