Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 8:28-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Cifukwa cace Yesu anati, Pamene mutadzamkweza Mwana wa munthu, pomwepo mudzazindikira kuti Ine ndine, ndipo sindicita kanthu kwa Ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.

29. Ndipo wondituma Ine ali ndi Ine; sanandisiya Ine pa ndekha; cifukwa ndicita Ine rimene zimkondweretsa iye nthawi zonse.

30. Pakulankhula iye zimenezi, ambiri anakhulupirira iye.

31. Cifukwa cace Yesu ananena kwa Ayuda aja adakhulupirira iye, Ngati mukhala inu m'mau anga, muli akuphunzira anga ndithu;

32. ndipo mudzazindikira coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani.

33. Anamyankha iye, Tiri mbeu ya Abrahamu, ndipo sitinakhala akapolo a munthu nthawi iri yonse; munena bwanji; Mudzayesedwa aufulu?

34. Yesu anayankha iwo, nati, Indetu, indetu, ndinena kwa inu kuti yense wakucita cimo ali kapolo wa cimolo.

35. Koma kapolo sakhala m'nyumba nthawi yonse; mwana ndiye akhala nthawi yonse.

36. Cifukwa cace ngati Mwana adzakuyesani inu aufulu, mudzakhala mfulu ndithu.

37. Ndidziwa kuti muli mbeu ya Abrahamuj koma mufuna kundipha Ine, cifukwa mau anga alibe malo mwa inu.

Werengani mutu wathunthu Yohane 8