Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 8:25-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Pamenepo ananena kwa iye, Ndinu yani? Yesu anati kwa iwo, Cimene comwe ndidalankhulanso ndi inu kuyambira paciyambi.

26. Ndiri nazo zambiri zakulankhula ndi zakuweruza za inu; koma wondituma Ine ali woona; ndipo zimene ndazimva kwa iye, zomwezo ndilankhuia kwa dziko lapansi.

27. Sanazindikira iwo kuti analikunena nao za Atate.

28. Cifukwa cace Yesu anati, Pamene mutadzamkweza Mwana wa munthu, pomwepo mudzazindikira kuti Ine ndine, ndipo sindicita kanthu kwa Ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.

29. Ndipo wondituma Ine ali ndi Ine; sanandisiya Ine pa ndekha; cifukwa ndicita Ine rimene zimkondweretsa iye nthawi zonse.

30. Pakulankhula iye zimenezi, ambiri anakhulupirira iye.

31. Cifukwa cace Yesu ananena kwa Ayuda aja adakhulupirira iye, Ngati mukhala inu m'mau anga, muli akuphunzira anga ndithu;

32. ndipo mudzazindikira coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani.

33. Anamyankha iye, Tiri mbeu ya Abrahamu, ndipo sitinakhala akapolo a munthu nthawi iri yonse; munena bwanji; Mudzayesedwa aufulu?

34. Yesu anayankha iwo, nati, Indetu, indetu, ndinena kwa inu kuti yense wakucita cimo ali kapolo wa cimolo.

35. Koma kapolo sakhala m'nyumba nthawi yonse; mwana ndiye akhala nthawi yonse.

Werengani mutu wathunthu Yohane 8