Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 8:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma Yesu anamuka ku phiri la Azitona.

2. Komac mamawa anadzanso kuKacisi, ndipo anthu onse anadza kwa iye; ndipo m'mene anakhala pansi anawaphunzitsa.

3. Koma alembi ndi Afarisi anabwera naye kwa iye mkazi wogwidwa m'cigololo, ndipo pamene anamuimika iye pakati,

4. ananena kwa iye, Mphunzitsi, mkazi uyu wagwidwa alimkucita cigololo.

5. Koma m'cilamulo Mose anatilamulira, ttwaponye miyala otere. Cifukwa cace Inu munena ciani za iye?

6. Koma ici ananena kuti amuyese iye, kuti akhale naco comneneza iye. Koma Yesu, m'mene adawerama pansi analemba pansi ndi cala cace.

7. Koma pamene anakhalakhala alikumfunsabe iye, anaweramuka, nati kwa iwo, Amene mwa inu ali wopanda cimo, ayambe kumponya mwala,

8. Ndipo m'mene adaweramanso analemba ndi cala cace pansi.

9. Koma iwo, m'mene adamva, anaturukamo amodzi amodzi, kuyambira akulu, kufikira otsiriza; ndipo Yesu anatsala yekha, ndi mkazi, alikuima pakati.

10. Koma Yesu pamene adaweramuka, anati kwa iye, Mkazi iwe, ali kuti ajawa? Palibe munthu anakutsutsa kodi?

Werengani mutu wathunthu Yohane 8