Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 7:45-53 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

45. Pamenepo anyamatawo anadza kwa ansembe akulu ndi Afarisi; ndipo iwowa anati kwa iwo, Simunamtenga iye bwanji?

46. Anyamatawo anayankha, 7 Nthawi yonse palibe munthu analankhula cotero.

47. Pamenepo Afarisi anayankha iwo, Kodi mwasokeretsedwa inunso?

48. 8 Kodi wina wa akuru anakhulupirira iye, kapena wa Afarisi?

49. Koma khamu ili losadziwa cilamulo, likhala lotembereredwa.

50. 9 Nikodemo ananena kwa iwo, amene uja adadza kwa iye kale, ali mmodzi wa iwo,

51. Kodi cilamulo cathu ciweruza munthu, osayamba kumva iye, ndi kuzindikira cimene, acita?

52. Anayankha nati kwa iye, Kodi iwenso uli woturuka m'Galileya? Santhula, nuone kuti m'Galileya sanauka mneneri.

53. Ndipo anamuka munthu yense ku nyumba yace.

Werengani mutu wathunthu Yohane 7