25. Pamenepo ena a iwo a ku Yerusalemu ananena, Kodi suyu amene afuna kumupha r
26. ndipo taona amalankhula poyera, ndipo sanena kanthu kwa iye. Kapena kodi akuru adziwa ndithu kuti ndiye Kristu ameneyo?
27. Koma ameneyo tidziwa uko acokera: koma Kristu pamene akadzadza, palibe mmodzi adzadziwa uko acokera.
28. Pamenepo Yesu anapfuula m'Kacisi, alikuphunzitsa ndi kunena, Mundidziwa Ine, ndiponso mudziwa uko ndicokera; ndipo sindinadza Ine ndekha, koma iye wondituma Ine amene inu simumdziwa, ali woona.
29. Ine ndimdziwa iye; cifukwa ndiri wocokera kwa iye, nandituma Ine Iyeyu.
30. Pamenepo anafuna kumgwira iye; koma palibe wina anamgwira kumanja, cifukwa nthawi yace siinafike.
31. Koma ambiri a m'khamu la anthu anakhulupirira iye; ndipo ananena, Pamene Kristu akadza kodi adzacita zizindikilo zambiri zoposa zimene adazicita ameneyo?
32. Afarisi anamva khamu la anthu ling'ung'udza zimenezi za iye; ndipo ansembe akulu ndi Afarisi anatuma anyamata kuti akamgwire iye.
33. Pamenepo Yesu anati, Katsala kanthawi ndiri ndi inu, ndipo ndimuka kwa iye wondituma Ine.
34. Mudzafunafuna Ine, osandipeza; ndipo pomwe ndiri Ine, inu simungathe kudzapo.