Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 7:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo zitapita izi Yesu anayendayenda m'Galileya; pakuti sanafuna kuyendayenda m'Yudeya, cifukwa Ayuda anafuna kumupha iye.

2. Koma phwando la Ayuda, phwando la misasa, linayandikira.

3. Cifukwa cace abale ace anati kwa iye, Cokani pano, mumuke ku Yudeya, kuti akuphunzita anunso akapenye nchito zanu zimenemucita.

4. Pakuti palibe munthu acita kanthu mobisika, nafuna yekha kukhala poyera, Ngati mucita izi, dzionetsereni eni nokha kwa dziko lapansi,

5. Pakuti angakhale abale ace sanakhulupirira iye.

6. Cifukwa cace Yesu ananena nao, Nthawi yanga siinafike; koma nthawi yanu yakonzeka masiku onse.

7. Dziko lapansi silingathe kudana ndi inu; koma Ine lindida popeza Ine ndilicitira umboni, kuti nchito zace ziri zoipa,

Werengani mutu wathunthu Yohane 7