Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 6:7-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Filipo anayankha iye, Mikate ya marupiya atheka mazana awiri siikwanira iwo, kuti yense atenge pang'ono.

8. Mmodzi wa akuphunzira ace, Andreya, mbale wace wa Simoni Petro, ananena ndi Iye,

9. Pali mnyamata pano, amene ali nayo mikate isanu yabarele, ndi tinsomba tiwiri; koma nanga izi zifikira bwanji ambiri otere?

10. N ati Yesu, Akhalitseni anthu pansi, Ndipo panali udzu wambiri pamalopo, Pamenepo amunawo anakhala pansi, kuwerenga kwao monga zikwi zisanu.

11. Pomwepo Yesu anatenga mikateyo; ndipo pamene adayamika, anagawira iwo akukhala pansi; momwemonso ndi tinsomba, monga momwe iwo anafuna.

12. Ndipo pamene adakhuta, Iyeananena kwa akuphunzira ace, Sonkhanitsani makombo kuti kasatayike kanthu.

13. Pomwepo anasonkhanitsa, nadzaza mitanga khumi ndi iwiri ndi makombo a mikate isanuyo yabarele, amene anatsalira anadyawo.

14. Cifukwa cace, anthu, poona cizindikilo cimene anacita, ananena, kuti, Ameneyo ndiye mneneri ndithu wakudzayom'dziko lapansi.

15. Pamenepo Yesu, pozindikira kuti alikufuna kudza kudzamgwira iye, kuti amlonge ufumu, anacokanso kunka kuphiri pa yekha.

16. Koma pofika madzulo, akuphunzira ace anatsikira kunyanja;

17. ndipo pamene adalowa m'ngalawa, analikuoloka nyanja kunka ku Kapernao. Ndipo kutada pamenepo, koma Yesu asanadze kwa iwo.

18. Ndipo nyanja inalikuuka cifukwa ca mphepo yaikulu yakuombako.

19. Ndipo parnene adapalasa monga mastadiya makumi awiri ndi asanu kapena makumi atatu, anaona Yesu alikuyenda panyanja, ndi kuyandikira ngalawa; ndipo anacita mantha.

20. Koma iye ananena nao, ndine; musaope.

21. Pamenepo analola kumlandira m'ngalawa; ndipo pomwepo ngalawayo inafika kumtunda kumene analikunkako.

22. M'mawa mwace khamu la anthu limene linaima tsidya lija la nyanja linaona kuti palibe ngalawa yina koma imodzi, ndi kuti Yesu sanalowa pamodzi ndi akuphunzira ace m'ngalawamo, koma akuphunzira ace adacoka pa okha;

23. koma zinacokera ngalawa zina ku Tiberiya, pafupi pa malo pomwe adadyapo mkate m'mene Yesu adayamika;

24. cifukwa cace pamene khamu la anthu linaona kuti palibe Yesu, ndi akuphunzira ace palibe, iwo okha analowa m'ngalawazo nadza ku Kapernao, alikufuna Yesu.

Werengani mutu wathunthu Yohane 6