Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 6:66-71 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

66. 19 Pa ici ambiri a akuphunzira ace anabwerera m'mbuyo, ndipo sanayenda-yendanso ndi iye.

67. Cifukwa cace Yesu anati kwa khumi ndi awiriwo, Nanga inunso mufuna kucoka?

68. Simoni Petro anamyankha iye, Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nao mau a moyo wosatha.

69. Ndipo 20 ife tikhulupirira, ndipo tidziwa kuti Inu ndinu Woyera wa Mulungu.

70. Yesu anayankha iwo, 21 Kodi sindinakusankhani khumi ndi awiri, ndipo mwa inu 22 mmodzi ali mdierekezi?

71. Koma adanena za Yudase, mwana wa Simoni Isikariote, pakuti iye ndiye amene akampereka iye, ali mmodzi wa khumi ndi awiri.

Werengani mutu wathunthu Yohane 6