Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 6:53-65 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

53. Cifukwa cace Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinenandi inu, 10 Ngati simukudya thupi la Mwana wa munthu ndi kumwa mwazi wace, mulibe moyo mwa inu nokha.

54. 11 Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomariza.

55. Pakuti thupi langa ndi cakudya ndithu, ndi mwazi wanga ndi caku mwa ndithu.

56. Iye wakudya thupi langa indi kumwa mwazi wanga 12 akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye.

57. Monga Atate wamoyo anandituma Ine, ndipo Inenso ndiri ndi moyo cifukwa ca Atate; momwemo wondidya Ine, iyeyu adzakhala ndi moyo cifukwa ca Ine.

58. 13 Mkate wotsika Kumwamba ndi umenewu: si monga makolowo, anadya namwalira; iye wakudya mkate umene adzakhala ndi moyo nthawi zonse.

59. Izi ananena m'sunagoge, pakuphunzitsa m'Kapernao.

60. 14 Pamenepo ambiri a akuphunzira ace, pakumva izi, anati, Mau awa ndi osautsa; akhoza kumva awa ndani?

61. Koma Yesu podziwa mwa yekha kuti akuphunzira ace alikung'ung'udza cifukwa ca ici, anati kwa iwo, ici mukhumudwa naco?

62. 15 Nanga bwanji ngati mukaona Mwana wa munthu alikukwera kumene anali kale lomwe?

63. 16 Wopatsa moyo ndi mzimu; thupi silithandiza konse. Mau amene ndalankhula ndi inu ndiwo mzimu, ndi moyo.

64. Koma 17 pali ena mwa inu amene sakhuluplra, Pakuti. Yesu anadziwa poyamba amene ali osakhulupira, ndi amene adzampereka.

65. Ndipo ananena, 18 Cifukwa ca ici ndinati kwa inu, kuti palibe munthu angathe kudza kwa Ine, koma ngati kupatsidwa kwa Iye ndi Atate.

Werengani mutu wathunthu Yohane 6