Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 6:3-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Koma Yesu anakwera kuphiri, nakhala pansi komweko pamodzi ndi akuphunzira ace.

4. Ndipo Paskha, phwando la Ayuda, anayandikira.

5. Pamenepo Yesu, pokweza maso ace, ndi kuona kuti khamu lalikuru lirinkudza kwa iye, ananena kwa Filipo, Tidzagula kuti mikate kuti adye awa?

6. Koma ananena ici kuti amuyese; pakuti anadziwa yekha cimene adzacita.

7. Filipo anayankha iye, Mikate ya marupiya atheka mazana awiri siikwanira iwo, kuti yense atenge pang'ono.

8. Mmodzi wa akuphunzira ace, Andreya, mbale wace wa Simoni Petro, ananena ndi Iye,

9. Pali mnyamata pano, amene ali nayo mikate isanu yabarele, ndi tinsomba tiwiri; koma nanga izi zifikira bwanji ambiri otere?

Werengani mutu wathunthu Yohane 6