Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 6:19-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo parnene adapalasa monga mastadiya makumi awiri ndi asanu kapena makumi atatu, anaona Yesu alikuyenda panyanja, ndi kuyandikira ngalawa; ndipo anacita mantha.

20. Koma iye ananena nao, ndine; musaope.

21. Pamenepo analola kumlandira m'ngalawa; ndipo pomwepo ngalawayo inafika kumtunda kumene analikunkako.

22. M'mawa mwace khamu la anthu limene linaima tsidya lija la nyanja linaona kuti palibe ngalawa yina koma imodzi, ndi kuti Yesu sanalowa pamodzi ndi akuphunzira ace m'ngalawamo, koma akuphunzira ace adacoka pa okha;

23. koma zinacokera ngalawa zina ku Tiberiya, pafupi pa malo pomwe adadyapo mkate m'mene Yesu adayamika;

24. cifukwa cace pamene khamu la anthu linaona kuti palibe Yesu, ndi akuphunzira ace palibe, iwo okha analowa m'ngalawazo nadza ku Kapernao, alikufuna Yesu.

25. Ndipo pamene anampeza iye tsidya lina la nyanja, anati kwa iye, Rabi, munadza kuno liti?

Werengani mutu wathunthu Yohane 6