Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 6:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Zitapita izi anacoka Yesu kunka ku tsidya lija la nyanja ya Galileya, ndiyo ya Tiberiya,

2. Ndipo khamu lalikuru la anthu linamtsata iye, cifukwa anaona zizindikilo zimene anacita pa odwala.

3. Koma Yesu anakwera kuphiri, nakhala pansi komweko pamodzi ndi akuphunzira ace.

4. Ndipo Paskha, phwando la Ayuda, anayandikira.

5. Pamenepo Yesu, pokweza maso ace, ndi kuona kuti khamu lalikuru lirinkudza kwa iye, ananena kwa Filipo, Tidzagula kuti mikate kuti adye awa?

6. Koma ananena ici kuti amuyese; pakuti anadziwa yekha cimene adzacita.

7. Filipo anayankha iye, Mikate ya marupiya atheka mazana awiri siikwanira iwo, kuti yense atenge pang'ono.

8. Mmodzi wa akuphunzira ace, Andreya, mbale wace wa Simoni Petro, ananena ndi Iye,

9. Pali mnyamata pano, amene ali nayo mikate isanu yabarele, ndi tinsomba tiwiri; koma nanga izi zifikira bwanji ambiri otere?

10. N ati Yesu, Akhalitseni anthu pansi, Ndipo panali udzu wambiri pamalopo, Pamenepo amunawo anakhala pansi, kuwerenga kwao monga zikwi zisanu.

11. Pomwepo Yesu anatenga mikateyo; ndipo pamene adayamika, anagawira iwo akukhala pansi; momwemonso ndi tinsomba, monga momwe iwo anafuna.

12. Ndipo pamene adakhuta, Iyeananena kwa akuphunzira ace, Sonkhanitsani makombo kuti kasatayike kanthu.

Werengani mutu wathunthu Yohane 6