Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 5:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Zitapita izi panali phwando la Ayuda; ndipo Yesu anakwera kunka ku Yerusalemu.

2. Koma pali thamanda m'Yerusalemu pa cipata ca nkhosa, lochedwa m'Cihebri Betesda, liri ndi makumbi asanu.

3. M'menemo munagona khamu lalikuru la anthu odwala akhungu, opunduka miyendo, opuwala. [

4. ]

5. Koma panali munthu wina apo, ali m'kudwala kwace zaka makumi atatu kudza zisanu ndi zitatu.

6. Yesu, pakuona ameneyo alikugona, ndipo anadziwa kuti anatero nthawi yaikuru pamenepo, ananena naye, Ufuna kuciritsidwa kodi?

7. Wodwalayo anayankha, Ambuye, ndiribe wondibvika ine m'thamanda, pali ponse madzi abvundulidwa; koma m'mene ndirinkudza ine, wina atsika ndisanatsike ine.

8. Yesu ananena naye, Tauka, yalula mphasa yako, nuyende,

9. Ndipo pomwepo munthuyu anacira, nayalula mphasa yace, nayenda.Koma tsiku lomwelo linali la Sabata.

10. Cifukwa cace Ayuda ananena kwa wociritsidwayo, Ndi Sabata, ndipo sikuloledwa kwa iwe kuyalula mphasa yako.

Werengani mutu wathunthu Yohane 5