Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 4:9-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Pamenepo mkazi wa m'Samariya ananena ndi iye, Bwanji Inu, muli Myuda, mupempha kwa ine kumwa, ndine mkazi Msamariya? (pakuti Ayuda sayenderana nao Asamariya),

10. Yesu anayankha nati kwa iye, Ukadadziwa mtulo wa Mulungu, ndi Iye amene alinkunena ndi iwe, Undipatse Ine ndimwe; ukadapempha iye, ndipo akadakupatsa madzi amoyo.

11. Mkaziyo ananena ndi Iye, Ambuye, mulibe cotungira madzi, ndi citsime ciri cakuya; ndipo mwatenga kuti madzi amoyo?

12. kodi muli wamkuru ndi atate wathu Yakobo amene anatipatsa ife citsimeci, namwamo iye yekha, ndi ana ace, ndi zoweta zace?

13. Yesu anayankha nati kwa iye, Yense wakumwako madzi awa adzamvanso Iudzu;

14. koma iye wakumwa madzi amene Ine ndidzampatsa sadzamva ludzu nthawi zonse; koma madzi amene Ine ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira ku moyo wosatha.

15. Mkaziyo ananena kwa iye, Ambuye, ndipatseni madzi amene, kuti ndisamve ludzu, kapena ndisadze kuno kudzatunga.

16. Yesu ananena kwa iye, Muka, kamuitane mwamuna wako, nudze kuno.

17. Mkazi anayankha nati kwa iye, Ndiribe mwamuna. Yesu ananena naye, Wanena bwino, kuti mwamuna ndiribe;

18. pakuti wakhala nao amuna asanu; ndipo iye amene ukhala nave tsopano sali mwamuna wako; ici wanena zoona.

19. Mkazi ananena ndi iye, Ambuye, ndizindikira kuti muli Mneneri.

Werengani mutu wathunthu Yohane 4