Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 4:5-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Cifukwa cace anadza ku mudzi wa Samariya, dzina lace Sukari, pafupi pa kadziko kamene Yakobo adapatsa mwana wace Yosefe;

6. ndipo pamenepo panali citsime ca Yakobo. Ndipo Yesu, popeza analema ndi ulendo wace, motero anakhala pacitsime,

7. Kunali ngati ora lacisanu ndi cimodzi. Kunadza mkazi woturuka m'Samariya kudzatunga madzi. Yesu ananena naye, Undipatse Ine ndimwe.

8. Pakuti ophunzira ace adacoka kunka kumudzi kuti akagule cakudya.

9. Pamenepo mkazi wa m'Samariya ananena ndi iye, Bwanji Inu, muli Myuda, mupempha kwa ine kumwa, ndine mkazi Msamariya? (pakuti Ayuda sayenderana nao Asamariya),

10. Yesu anayankha nati kwa iye, Ukadadziwa mtulo wa Mulungu, ndi Iye amene alinkunena ndi iwe, Undipatse Ine ndimwe; ukadapempha iye, ndipo akadakupatsa madzi amoyo.

11. Mkaziyo ananena ndi Iye, Ambuye, mulibe cotungira madzi, ndi citsime ciri cakuya; ndipo mwatenga kuti madzi amoyo?

12. kodi muli wamkuru ndi atate wathu Yakobo amene anatipatsa ife citsimeci, namwamo iye yekha, ndi ana ace, ndi zoweta zace?

13. Yesu anayankha nati kwa iye, Yense wakumwako madzi awa adzamvanso Iudzu;

14. koma iye wakumwa madzi amene Ine ndidzampatsa sadzamva ludzu nthawi zonse; koma madzi amene Ine ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira ku moyo wosatha.

15. Mkaziyo ananena kwa iye, Ambuye, ndipatseni madzi amene, kuti ndisamve ludzu, kapena ndisadze kuno kudzatunga.

16. Yesu ananena kwa iye, Muka, kamuitane mwamuna wako, nudze kuno.

17. Mkazi anayankha nati kwa iye, Ndiribe mwamuna. Yesu ananena naye, Wanena bwino, kuti mwamuna ndiribe;

18. pakuti wakhala nao amuna asanu; ndipo iye amene ukhala nave tsopano sali mwamuna wako; ici wanena zoona.

19. Mkazi ananena ndi iye, Ambuye, ndizindikira kuti muli Mneneri.

20. Makolo athu analambira m'phiri ili; ndipo inu munena, kuti m'Yerusalemu muli malo ozenera kulambiramo anthu.

21. Yesu ananena naye, Tamvera Ine, mkazi iwe, kuti ikudza nthawi, imene simudzalambira Atate kapena m'phiri ili, kapena m'Yerusalemu.

22. Inu mulambira cimene simucidziwa; ife tilambira cimene ticidziwa; pakuti cipulumutso cicokera kwa Ayuda.

23. Koma ikudza nthawi, ndipo tsopano iripo, imene olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m'coonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ace.

Werengani mutu wathunthu Yohane 4