Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 4:38-48 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

38. Ine ndinatuma inu kukamweta cimene simunagwirirapo nchito: ena anagwira nchito, ndipo inu mwalowa nchito yao.

39. Ndipo m'mudzi mula anthu Asamariya ambiri anamkhulupirira iye cifukwa ca mau a mkazi, wocita umboniyo, kuti, Anandiuza ine zinthu ziri zonse ndinazicita.

40. Cifukwa cace pamene Asamariya anadza kwa iye, anamfunsa akhale nao; ndipo anakhala komweko masiku awiri.

41. Ndipo ambiri oposa anakhulupira cifukwa ca mau ace:

42. ndipo ananena kwa mkazi, kuti, Tsopano sitikhulupira cifukwa ca kulankhula kwako: pakuti tamva tokha, ndipo tidziwa kuti Mpulumutsi wa dziko lapansi ndi Iyeyu ndithu.

43. Koma atapita masiku awiriwo anacoka komweko kunka ku Galileya.

44. Pakuti Yesu mwini anacita umboni kuti, Mneneri alibe ulemu m'dziko la kwao.

45. Cifukwa cace pamene anadza ku Galileya, Agalileva anamlandira iye, atakaona zonse zimene anazicita m'Yerusalemu paphwando; pakuti iwonso ananka kuphwando.

46. Cifukwa cace Yesu anadzanso ku Kana wa m'Galileya, kumene anasandutsa madzi vinyo. Ndipo kunalimkulu wina wa mfumu, mwana wace anadwala m'Kapernao.

47. Iyeyu, pamene anamva kuti Yesu wacokera ku Yudeya nafika ku Galileya, ananka kwa iye, nampempha kuti atsike kukaciritsa mwana wace; pakuti anali pafupi imfa.

48. Pamenepo Yesu anati kwa iye, Ngati simuona zizindikilo ndi zozizwa, simudzakhulupira.

Werengani mutu wathunthu Yohane 4