Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 4:27-39 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Ndipo pamenepo anadza ophunzira ace; nazizwa kuti analinkulankhula ndi mkazi; koma panalibe wina anati, Mufuna ciani? kapena, mulankhula naye ciani?

28. Pamenepo mkazi anasiya mtsuko wace, namuka kumudzi, nanena ndi anthu,

29. Tiyeni, mukaone munthu, amene anandiuza zinthu ziri zonse ndinazicita: ameneyu sali Kristu nanga?

30. Anaturuka iwo m'mudzi ndipo analinkudza kwa iye.

31. Pa mphindikati iyi ophunzira ace anampempha iye, ndi kunena, Rabi, idyani.

32. Koma iye anati kwa iwo, Ine ndiri naco cakudya cimene inu simucidziwa.

33. Cifukwa cace ophunzira ananena wina ndi mnzace, Kodi pali wina anamtengera iye kanthu kakudya?

34. Yesu ananena nao, Cakudya canga ndico kuti ndicite cifuniro ca iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza nchito yace.

35. Kodi simunena inu, kuti, Yatsala miyezi inai, ndipo kudza kumweta? Onani ndinena kwa inu, Kwezani maso anu, nimuyang'ane m'minda, kuti mwayera kale kufikira kumweta.

36. Wakumweta alandira kulipira, nasonkhanitsira cobala ku moyo wosatha; kuti wofesayo akakondwere pamodzi ndi womwetayo.

37. Pakuti m'menemo conenaco ciri coona, Wofesa ndi wina, womweta ndi winanso.

38. Ine ndinatuma inu kukamweta cimene simunagwirirapo nchito: ena anagwira nchito, ndipo inu mwalowa nchito yao.

39. Ndipo m'mudzi mula anthu Asamariya ambiri anamkhulupirira iye cifukwa ca mau a mkazi, wocita umboniyo, kuti, Anandiuza ine zinthu ziri zonse ndinazicita.

Werengani mutu wathunthu Yohane 4