Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 4:19-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Mkazi ananena ndi iye, Ambuye, ndizindikira kuti muli Mneneri.

20. Makolo athu analambira m'phiri ili; ndipo inu munena, kuti m'Yerusalemu muli malo ozenera kulambiramo anthu.

21. Yesu ananena naye, Tamvera Ine, mkazi iwe, kuti ikudza nthawi, imene simudzalambira Atate kapena m'phiri ili, kapena m'Yerusalemu.

22. Inu mulambira cimene simucidziwa; ife tilambira cimene ticidziwa; pakuti cipulumutso cicokera kwa Ayuda.

23. Koma ikudza nthawi, ndipo tsopano iripo, imene olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m'coonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ace.

24. Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m'coonadi.

25. Mkazi ananena ndi Iye, Ndidziwa kuti Mesiya adza (wochedwa Kristu): akadzadza Iyeyu, adzatiuza zonse.

26. Yesu ananena naye, Ine wakulankhula nawe ndine amene.

27. Ndipo pamenepo anadza ophunzira ace; nazizwa kuti analinkulankhula ndi mkazi; koma panalibe wina anati, Mufuna ciani? kapena, mulankhula naye ciani?

28. Pamenepo mkazi anasiya mtsuko wace, namuka kumudzi, nanena ndi anthu,

29. Tiyeni, mukaone munthu, amene anandiuza zinthu ziri zonse ndinazicita: ameneyu sali Kristu nanga?

30. Anaturuka iwo m'mudzi ndipo analinkudza kwa iye.

Werengani mutu wathunthu Yohane 4