Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 3:29-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Iye amene ali naye mkwatibwi ali mkwati, koma mnzace wa mkwatiyo, wakuimirira ndi kumvera iye, akondwera kwakukuru cifukwa ca mau a mkwatiyo; cifukwa cace cimwemwe canga cimene cakwanira.

30. Iyeyo ayenera kukula koma ine ndicepe.

31. Iye wocokera Kumwamba ali woposa onse; iye amene ali wa dziko lapansi ali wa dziko lapansi, nalankhula za dziko lapansi: Iye wocokera Kumwamba ali woposa onse.

32. Cimene anaciona nacimva, acita umboni wa ici comwe; ndipo kulibe munthu alandira umboni wace.

33. 1 Iye amene analandira umboni wace anaikapo cizindikilo cace kuti Mulungu ali woona.

34. Pakuti 2 Iye amene Mulungu anamtuma alankhula mau a Mulungu; pakuti 3 sapatsa Mzimu ndi muyeso.

35. 4 Atate akonda Mwana, nampatsa zinthu zonse m'dzanja lace.

36. Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nao moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.

Werengani mutu wathunthu Yohane 3