Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 3:2-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wocokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kucita zizindikilo zimene inu mucita, ngati Mulungu sakhala naye,

3. Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona Ufumu wa Mulungu.

4. Nikodemoananena kwa iye, Munthu akhoza bwanji kubadwa atakalamba? Kodi akhoza kulowanso m'mimba ya amace ndi kubadwa?

5. Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu.

6. Cobadwa m'thupi cikhala thupi, ndipo cobadwa mwa Mzimu, cikhala mzimu.

7. Usadabwe cifukwa ndinati kwa iwe, Uyenera kubadwa mwatsopano.

8. Mphepo iomba pomwe ifuna, ndipo ukumva mau ace, komavsudziwa, kumene icokera, ndi kumene imuka; cotero ali yense wobadwa mwa Mzimu.

9. Nikodemo anayankha nati kwa iye, Izi zingatheke bwanji?

Werengani mutu wathunthu Yohane 3