Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 20:4-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Koma anathamanga onse awiri pamodzi; ndipo wophunzira winayo anathamanga naposa Petro, nayamba kufika kumanda;

5. ndipo m'mene anawerama cosuzumira anaona nsaru zabafuta zitakhala, komatu sanalowamo.

6. Pamenepo anadzanso Simoni Petro alikumtsata iye, nalowa m'manda; ndipo anaona nsaru zabafuta zitakhala,

7. ndi mlezo, umene unali pamutu pace, wosakhala pamodzi ndi nsaru zabafuta, koma wopindika padera pamalo pena.

8. Pamenepo tsono analowanso wophunzira winayo, amene anayamba kufika kumanda, ndipo anaona, nakhulupira.

9. Pakuti kufikira pomwepo sanadziwa lembo lakuti ayenera iye kuuka kwa akufa.

10. Cifukwa cace akuphunzirawo anacokanso, kunka kwao.

11. Koma Mariya analikuima kumanda kunja, alikulira. Ndipo m'mene alikulira anawerama cisuzumirire kumanda;

12. ndipo anaona angelo awiri atabvala zoyera, alikukhala mmodzi kumutu, ndi wina kumiyendo, kumene mtembo wa Yesu udagona.

Werengani mutu wathunthu Yohane 20