Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 20:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma tsiku loyamba la Sabata anadza Mariya wa Magadala mamawa, kusanayambe kuca, kumanda, napenya mwala wocotsedwa kumanda.

2. Pomwepo anathamanga nadza kwa Simoni Petro ndi kwa wophunzira wina amene Yesu anamkonda, nanena nao, Anacotsa Ambuye kumanda, ndipo sitidziwa kumene anamuika iye.

3. Anaturuka tsono Petro ndi wophunzira winayo, nalinkupita kumanda.

4. Koma anathamanga onse awiri pamodzi; ndipo wophunzira winayo anathamanga naposa Petro, nayamba kufika kumanda;

5. ndipo m'mene anawerama cosuzumira anaona nsaru zabafuta zitakhala, komatu sanalowamo.

6. Pamenepo anadzanso Simoni Petro alikumtsata iye, nalowa m'manda; ndipo anaona nsaru zabafuta zitakhala,

7. ndi mlezo, umene unali pamutu pace, wosakhala pamodzi ndi nsaru zabafuta, koma wopindika padera pamalo pena.

8. Pamenepo tsono analowanso wophunzira winayo, amene anayamba kufika kumanda, ndipo anaona, nakhulupira.

9. Pakuti kufikira pomwepo sanadziwa lembo lakuti ayenera iye kuuka kwa akufa.

Werengani mutu wathunthu Yohane 20