Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 2:21-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Koma iye analikunena za kacisi wathupi lace.

22. Cifukwa cace atauka kwa akufa, akuphunzira ace anakumbukira kuti ananena ici; ndipo anakhulupirira colemba, ndi mau amene Yesu ananena.

23. Koma pamene anali m'Yerusalemu pa Paskha paphwando, ambiri anakhulupirira dzinalace, pakuona zizindikilo zace zimene anaeitazi.

24. Koma Yesu sanakhulupirira iwo kuti akhale nao, cifukwa iye anadziwa anthu onse,

25. ndipo sanasowa wina acite umboni za munthu; pakuti anadziwa iye yekha cimene cinali mwa munthu.

Werengani mutu wathunthu Yohane 2