Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 2:14-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo anapeza m'Kacisiiwo akugulitsa ng'ombe ndi nkhosa ndi nkhunda, ndi akusinthana ndalama alikukhala pansi.

15. Ndipo pamene adapanga mkwapulo wazingwe, anaturutsa onse m'Kacisimo, ndi nkhosa ndi ng'ombe; nakhuthula ndalama za osinthanawo, nagubuduza magome;

16. nati kwa iwo akugulitsa nkhunda, Cotsani izi muno; musamayesa nyumba ya Atate wanga nyumba ya malonda.

17. Akuphunzira ace anakumbukila kuti kunalembedwa, Cangu ca pa nyumba yanu candidya ine.

18. Cifukwa cace Ayuda anayankha nati kwa iye, Mutionetsera ife cizindikilo canji, pakuti mucita izi?

19. Yesu anayankha nati kwa iwo, Pasulani kacisi uyu, ndipo masiku atatu ndidzamuutsa.

20. Pamenepo Ayuda anati, Zaka makumi anai ndi zisanu ndi cimodzi analimkumanga Kacisiyu, kodi inu mudzamuutsa masiku atatu?

21. Koma iye analikunena za kacisi wathupi lace.

22. Cifukwa cace atauka kwa akufa, akuphunzira ace anakumbukira kuti ananena ici; ndipo anakhulupirira colemba, ndi mau amene Yesu ananena.

23. Koma pamene anali m'Yerusalemu pa Paskha paphwando, ambiri anakhulupirira dzinalace, pakuona zizindikilo zace zimene anaeitazi.

Werengani mutu wathunthu Yohane 2