Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 2:1-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo tsiku lacitatu pariali ukwati m'Kana wa m'Galileya; ndipo amace wa Yesu anali komweko.

2. Ndipo Yesu yemwe ndi akuphunzira ace anaitanidwa ku ukwatiwo.

3. Ndipo pakutha vinyo, amace wa Yesu ananena naye, Alibe vinyo,

4. Yesu nanena naye, Mkazi, ndiri ndi ciani ndi inu? nthawi yanga siinafike.

5. Amace ananena kwa atumiki, Cimene ciri conse akanena kwa inu, citani.

6. Ndipopanali pamenepo mitsuko yamiyala isanu ndi umodzi yoikidwako monga mwa mayeretsedwe a Ayuda, yonse ya miyeso iwiri kapena itatu.

7. Yesu ananena nao, Dzazani mitsukoyo ndi madzi. Naidzaza, nde nde nde.

8. Ndipo ananena nao, Tungani tsopano, mupite nao kwamkulu wa phwando. Ndipo anapita nao.

9. Koma pamene mkuluyo analawa madzi osanduka vinyowo, ndipo sanadziwa kumene anacokera (koma atumiki amene adatiinga madzi anadziwa), mkuluyo anaitana mkwati,

10. nanena naye, Munthu ali yense amayamba kuika vinyo wokoma; ndipo anthu atamwatu, pamenepo wina wosakoma; koma iwe wasunga vinyo wokoma kufikira tsopano lino.

11. Ciyambi ici ca zizindikilo zace Yesu anacita m'Kana wa m'Galileya naonetsera ulemerero wace; ndipo akuphunzira ace anakhulupirira iye.

12. Zitapita izianatsikira ku Kapemao, iye ndi amace, ndiabale ace, ndi ophunzira ace; nakhala komweko masiku owerengeka.

13. Ndipo Paskha wa Ayuda unayandikira, ndipo Yesu anakwera kunka ku Yerusalemu.

14. Ndipo anapeza m'Kacisiiwo akugulitsa ng'ombe ndi nkhosa ndi nkhunda, ndi akusinthana ndalama alikukhala pansi.

Werengani mutu wathunthu Yohane 2