Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 19:22-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Pilato anayankha, Cimene ndalemba, ndalemba.

23. Pamenepo asilikari, m'mene adapacika Yesu, anatenga zobvala zace, nadula panai, natenga wina cina, wina cina, ndiponso maraya; koma maraya anaombedwa monsemo kuyambira pamwamba pace, analibe msoko.

24. Cifukwa cace anati wina kwa mnzace, Tisang'ambe awa, koma ticite maere, awa akhale a yani; kuti lembo likwaniridwe limene linena, Anagawana zobvala zanga mwa iwo okha, ndi pa maraya anga anacitira maere. Ndipo asilikari anacita izi.

25. Koma pamtanda wa Yesu anaimirira amace, ndi mbale wa amace, Mariya, mkazi wa Kleopa, ndi Mariya wa Magadala.

26. Pamenepo Yesu pakuona amace, ndi wophunzira amene anamkonda, alikuimirirako, ananena kwa amace, Mkazi, taonani, mwana wanu!

Werengani mutu wathunthu Yohane 19