Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 19:12-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Pa ici Pilato anafuna kumasula iye; koma Ayuda anapfuula, ndi kunena, Ngati mumasula ameneyo, simuli bwenzi la Kaisara; yense wodziyesera yekha mfumu atsutsana naye Kaisara.

13. Pamenepo Pilato, m'mene adamva mau awa, anaturuka ndi Yesu, nakhala pansi pa mpando woweruzira kumalo dzina lace; Bwalo lamiyala, koma m'Cihebri, Gabata,

14. Koma linali tsiku lokonza Paskha; panali monga ora lacisanu ndi cimodzi. Ndipo ananena kwa Ayuda, Taonani, Mfumu yanu!

15. Pamenepo anapfuula iwowa, Cotsani, Cotsani, mpacikeni iye! Pilato ananena nao, Ndipacike Mfumu yanu kodi? Ansembe akulu anayankha, Tiribe Mfumu koma Kaisara.

16. Ndipo pamenepo anampereka iye kwa iwo kutiampacike,Pamenepo anatenga Yesu;

17. ndipo anasenza mtanda yekha, naturuka kunka ku malo ochedwa Maloa-bade, amene achedwa m'Cihebri, Golgota:

18. kumene anampacika Iye; ndipo pamodzi ndi iye awiri ena, cakuno ndi cauko, koma Yesu pakati.

19. Koma Pilato analemba lembo, naliika pamtanda. Koma panalembedwa, YESU MNAZARAYO, MFUMU YA AYUDA.

20. Ndipo lembo ilo analiwerenga ambiri a Ayuda; cifukwa malo amene Yesu anapaeikidwapo anali pafupipa mudziwo; ndipo linalembedwa m'Cihebri, ndi m'Ciroma, ndi m'Cihelene.

21. Pamenepo ansembe akulu a Ayuda, ananena kwa Pilato, Musalembe, Mfumu ya Ayuda; koma kuti Iyeyu anati, Ndiri Mfumu ya Ayuda.

Werengani mutu wathunthu Yohane 19