Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 18:5-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Anayankha iye, Yesu Mnazarayo. Yesu ananena nao, Ndine. Koma Yudase yemwe, wompereka iye, anaima nao pamodzi.

6. Ndipo m'mene anati kwa iwo, Ndine, anabwerera m'mbuyo, nagwa pansi.

7. Pamenepo anawafunsanso, Mufuna yani? koma iwo anati, Yesu Mnazarayo.

8. Yesu anayankha, Ndati, Ndine; cifukwa cace ngati mufuna Ine, lekani awa amuke;

9. kuti akwaniridwe mau amene ati, Mwa iwo amene mwandipatsa Ine, sindinataya mmodzi.

10. Pamenepo Simoni Petro pokhala nalo lupanga, analisolola nakantha kapolo wa mkulu wa ansembe, namsenga khutu lace lamanja. Koma dzina lace la kapoloyo ndiye Malko.

11. Pamenepo Yesu anati kwa Petro, Longa Iupanga m'cimakecace; cikho cimene Atate wandipatsa Ine sindimwere ici kodi?

12. Ndipo khamulo ndi kapitao wamkuru, ndi anyamata a Ayuda anagwira Yesu nammanga iye,

13. nayamba kupita naye kwa Anasi; pakuti anali mpongozi wa Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe caka comweco.

14. Koma Kayafa anali uja wakulangiza Ayuda, kuti kuyenera munthu mmodzi afere anthu.

15. Koma Simoni Petro ndi wophunzira wina anatsata Yesu. Koma wophunzira ameneyo anali wodziwika kwa mkulu wa ansembe, nalowa pamodzi ndi Yesu, m'bwalo la mkulu wa ansembe;

16. koma Petro anaima kukhomo kunja, Cifukwa cace wophunzira winayo amene anadziwika kwa mkulu wa ansembe, anaturuka nalankhula ndi wapakhomo, nalowetsa Petro.

17. Pamenepo namwali wapakhomoyo ananena kwa Petro, Kodi suli iwenso wa akuphunzira a munthu uyu? Iyeyu ananena, Sindine.

18. Koma akapolo ndi anyamata analikuimirirako, atasonkha mota wamakara; pakuti kunali kuzizira; ndipo analikuotha moto; koma Petronso anali nao alikuimirira ndi kuotha moto.

19. Ndipo mkulu wa ansembe anafunsa Yesu za akuphunzira ace, ndi ciphunzitso cace.

20. Yesu anayankha iye, Ine ndalankhula zomveka kwa dziko lapansi; ndinaphunzitsa Ine nthawi zonse m'sunagoge ndi m'Kacisi, kumene amasonkhana Ayuda onse; ndipo mobisika sindinalankhula kanthu.

21. Undifunsiranji Ine? funsa iwo amene adamva cimene ndinalankhula nao; taona, amenewo adziwa cimene ndinanena Ine.

Werengani mutu wathunthu Yohane 18