Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 18:18-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Koma akapolo ndi anyamata analikuimirirako, atasonkha mota wamakara; pakuti kunali kuzizira; ndipo analikuotha moto; koma Petronso anali nao alikuimirira ndi kuotha moto.

19. Ndipo mkulu wa ansembe anafunsa Yesu za akuphunzira ace, ndi ciphunzitso cace.

20. Yesu anayankha iye, Ine ndalankhula zomveka kwa dziko lapansi; ndinaphunzitsa Ine nthawi zonse m'sunagoge ndi m'Kacisi, kumene amasonkhana Ayuda onse; ndipo mobisika sindinalankhula kanthu.

21. Undifunsiranji Ine? funsa iwo amene adamva cimene ndinalankhula nao; taona, amenewo adziwa cimene ndinanena Ine.

22. Koma m'mene iye adanena izi, mmodzi wa anyamata akuimirirako anapanda Yesu khofu, ndi kuti, Kodi uyankha mkulu wa ansembe comweco?

Werengani mutu wathunthu Yohane 18