Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 18:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. M'mene Yesu adanena izi, anaturuka ndi akuphunzira ace, kunka tsidya lija la mtsinje wa Kedroni, kumene kunali munda, umene analowamo iye ndi akuphunzira ace.

2. Koma Yudasenso amene akampereka iye, anadziwa malowa; cifukwa Yesu akamkako kawiri kawiri ndi akuphunzira ace.

3. Pamenepo Yudase, m'mene adatenga gulu la asilikari ndi anyamata, kwa ansembe akulu ndi Afarisi, anadza komweko ndi nyali ndi miuni ndi zida.

4. Pamenepo Yesu, podziwa zonse zirinkudza pa iye, anaturuka, nati kwa iwo, Mufuna yani?

5. Anayankha iye, Yesu Mnazarayo. Yesu ananena nao, Ndine. Koma Yudase yemwe, wompereka iye, anaima nao pamodzi.

6. Ndipo m'mene anati kwa iwo, Ndine, anabwerera m'mbuyo, nagwa pansi.

7. Pamenepo anawafunsanso, Mufuna yani? koma iwo anati, Yesu Mnazarayo.

8. Yesu anayankha, Ndati, Ndine; cifukwa cace ngati mufuna Ine, lekani awa amuke;

9. kuti akwaniridwe mau amene ati, Mwa iwo amene mwandipatsa Ine, sindinataya mmodzi.

10. Pamenepo Simoni Petro pokhala nalo lupanga, analisolola nakantha kapolo wa mkulu wa ansembe, namsenga khutu lace lamanja. Koma dzina lace la kapoloyo ndiye Malko.

11. Pamenepo Yesu anati kwa Petro, Longa Iupanga m'cimakecace; cikho cimene Atate wandipatsa Ine sindimwere ici kodi?

12. Ndipo khamulo ndi kapitao wamkuru, ndi anyamata a Ayuda anagwira Yesu nammanga iye,

Werengani mutu wathunthu Yohane 18