Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 17:8-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. cifukwa mau amene munandipatsa Ine ndinapatsa iwo; ndipo analandira, nazindikira koona kuti ndinaturuka kwa Inu, ndipo anakhulupira kuti Inu munandituma Ine.

9. Ine ndiwapempherera iwo; sindipempherera dziko lapansi, koma iwo amene mwandipatsa Ine,

10. cifukwa ali anu: ndipo zanga zonse ziri zanu, ndi zanu ziri zanga; ndipo ndilemekezedwa mwa iwo.

11. Sindikhalanso m'dziko lapansi, koma iwo ali m'dziko lapansi, ndipo Ine ndidza kwa Inu. Atate. Woyera, sungani awa m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine, kuti akhale mmodzi, monga Ife.

12. Pamenendinakhala nao, Ine ndinalikuwasunga iwo m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayika mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa citayiko, kuti lembo likwaniridwe.

13. Koma tso pane ndidza kwa Inu; ndipo izi ndilankhula m'dziko lapansi, kuti akhale naco cimwemwe canga cokwaniridwa mwa iwo okha.

14. Ine ndawapatsa iwo mau anu; ndipo dziko lapansi linadana nao, cifukwa sakhala a dziko lapansi, monga Ine sindikhala wa dziko lapansi.

15. Sindipempha kuti muwacotse iwo m'dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo.

16. Siali adziko lapansi monga Ine sindiri wa dziko lapansi.

17. Patulani iwo m'coonadi; mau anu ndi coonadi.

18. Monga momwe munandituma Ine ku dziko lapansi, Inenso ndinatuma iwo ku dziko lapansi,

19. Ndipo cifukwa ca iwo Ine ndidzipatula ndekha kuti iwonso akhale opatulidwa m'coonadi.

20. Koma sindipempherera iwo okha, komanso iwo akukhulupirira Ine cifukwa ca mau ao;

Werengani mutu wathunthu Yohane 17