Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 17:6-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndalionetsera dzina lanu kwa anthu amene mwandipatsa Ine m'dziko lapansi; anali anu, ndipo mwandipatsa Ine iwo; ndipo adasunga mau anu.

7. Azindikira tsopane kuti zinthu ziri zonse zimene mwandipatsa Ine zicokera kwa Inu;

8. cifukwa mau amene munandipatsa Ine ndinapatsa iwo; ndipo analandira, nazindikira koona kuti ndinaturuka kwa Inu, ndipo anakhulupira kuti Inu munandituma Ine.

9. Ine ndiwapempherera iwo; sindipempherera dziko lapansi, koma iwo amene mwandipatsa Ine,

10. cifukwa ali anu: ndipo zanga zonse ziri zanu, ndi zanu ziri zanga; ndipo ndilemekezedwa mwa iwo.

Werengani mutu wathunthu Yohane 17