Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 17:20-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Koma sindipempherera iwo okha, komanso iwo akukhulupirira Ine cifukwa ca mau ao;

21. kuti onse akakhale amodzi, monga Inu Atate mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, kuti iwonso akakhale mwa Ife: kuti dziko lapansi likakhulupire kuti Inu munandituma Ine.

22. Ndipo ulemerero umene mwandipatsa Ine ndapatsa Iwo; kuti akhale amodzi, monga Ife tiri mmodzi;

23. Ine mwa iwo, ndi Inu mwa Ine, kuti akhale angwiro mwa mmodzi; kutr dziko lapansi lizindikire kuti Inu munandituma Ine, nimunawakonda iwo, monga momwe munakonda Ine,

24. 1 Atate, amene mwandipatsa Ine, ndifuna kuti, kumene ndiri Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang'anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; 2 pakuti munandikonda Inelisanakhazildke dziko lapansi.

25. Atate wolungama, 3 dziko lapansi silinadziwa Inu, koma 4 Ine ndinadziwa Inu; ndipo 5 iwo anazindikira kuti munandituma Ine;

26. ndipo 6 ndinazindikiritsa iwo dzina lanu, ndipo ndidzalizindikiritsa; kuti cikondi 7 cimene munandikonda naco cikhale mwa iwo, ndi Ine mwa iwo.

Werengani mutu wathunthu Yohane 17