Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 17:12-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Pamenendinakhala nao, Ine ndinalikuwasunga iwo m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayika mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa citayiko, kuti lembo likwaniridwe.

13. Koma tso pane ndidza kwa Inu; ndipo izi ndilankhula m'dziko lapansi, kuti akhale naco cimwemwe canga cokwaniridwa mwa iwo okha.

14. Ine ndawapatsa iwo mau anu; ndipo dziko lapansi linadana nao, cifukwa sakhala a dziko lapansi, monga Ine sindikhala wa dziko lapansi.

15. Sindipempha kuti muwacotse iwo m'dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo.

16. Siali adziko lapansi monga Ine sindiri wa dziko lapansi.

17. Patulani iwo m'coonadi; mau anu ndi coonadi.

18. Monga momwe munandituma Ine ku dziko lapansi, Inenso ndinatuma iwo ku dziko lapansi,

19. Ndipo cifukwa ca iwo Ine ndidzipatula ndekha kuti iwonso akhale opatulidwa m'coonadi.

20. Koma sindipempherera iwo okha, komanso iwo akukhulupirira Ine cifukwa ca mau ao;

21. kuti onse akakhale amodzi, monga Inu Atate mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, kuti iwonso akakhale mwa Ife: kuti dziko lapansi likakhulupire kuti Inu munandituma Ine.

22. Ndipo ulemerero umene mwandipatsa Ine ndapatsa Iwo; kuti akhale amodzi, monga Ife tiri mmodzi;

23. Ine mwa iwo, ndi Inu mwa Ine, kuti akhale angwiro mwa mmodzi; kutr dziko lapansi lizindikire kuti Inu munandituma Ine, nimunawakonda iwo, monga momwe munakonda Ine,

Werengani mutu wathunthu Yohane 17