Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 16:6-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Koma cifukwa ndalankhula izi ndi inu cisoni cadzala mumtima mwanu.

7. Koma ndinena Ine coonadi ndi inu; kuyenera kwa inu kuti ndicoke Ine; pakuti ngati sindicoka, Nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzamtuma iye kwa inu.

8. Ndipo atadza Iyeyo, adzatsutsa dziko lapansi za macimo, ndi za cilungamo, ndi za ciweruziro;

9. za macimo, cifukwa sakhulupirira Ine;

10. za cilungamo, cifukwa ndinka kwa Atate, ndipo simundionanso;

11. za ciweruziro, cifukwa mkuru wa dziko ili lapansi waweruzidwa.

12. Ndiri nazo zambirinso zakunena kwa inu, koma simungathe kuzisenza tsopano lino.

13. Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa coonadi, adzatsogolera inu m'coonadi conse; pakuti sadzalankhula za iye mwini; koma zinthu ziri zonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zirinkudza adzakulalikirani.

14. Iyeyo adzalemekeza Ine; cifukwa adzatenga za mwa Ine, nadzalalikira kwa inu.

15. Zinthu ziri zonse Atate ali nazo ndi zanga; cifukwa cace ndinati, kuti atenga za mwa Ine, nadzalalikira kwa inu.

16. Katsala kanthawi, ndipo simundionanso Ine, ndipo kanthawinso, ndipo mudzandiona Ine.

17. Mwa akuphunzira ace tsono anati wina ndi mnzace, ici nciani cimene anena ndi ife, Kanthawi ndipo simundiona; ndiponso kanthawi, ndipo mudzandiona; ndipo, cifukwa ndimuka kwa Atate?

Werengani mutu wathunthu Yohane 16