Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 16:25-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Zinthu izi ndalankhula ndi inu m'mafanizo; ikudza nthawi imene sindidzalankhula ndi inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu momveka za Atate.

26. Tsiku limenelo mudzapempha m'dzina langa; ndipo sindinena kwa inu kuti Ine ndidzafunsira inu kwa Atate;

27. pakuti Atate yekha akonda inu, cifukwa inu mwandikonda Ine, ndi kukhulupirira kuti Ine ndinaturuka kwa Atate.

28. Ndinaturuka mwa Atate, ndipo ndadza ku dziko lapansi: ndilisiyanso dziko lapansi, ndipo ndipita kwa Atate.

29. Akuphunzira ace ananena, Onani, tsopano mulankhula zomveka, ndipo mulibe kunena ciphiphiritso,

30. Tsopano tidziwa kuti mudziwa zonse, ndipo mulibe kusowa kuti wina akafunse Inu; mwa ici tikhulupirira kuti munaturuka kwa Mulungu.

31. Yesu anayankha iwo, Kodi mukhulupirira tsopano?

32. Onani ikudza nthawi, ndipo yafika, imene mudzabalalitsidwa, yense ku zace za yekha, ndipo mudzandisiya Ine pa ndekha. Ndipo sindikhala pa ndekha, cifukwa Atate ali pamodzi ndi Ine,

33. Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala naco cibvuto, koma limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi Ine.

Werengani mutu wathunthu Yohane 16